Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 19:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mose adakwera phiri kukakumana ndi Mulungu, ndipo Mulungu adamuitana m'phirimo namuuza kuti, “Uuze zidzukulu za Yakobe, ndiye kuti mtundu wonse wa Aisraele kuti,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:3
12 Mawu Ofanana  

Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera,


Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.


Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.”


Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa.


Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.”


Yehova ataona kuti Mose anapatuka kuti adzaonetsetse, Mulungu anamuyitana Mose kuchokera mʼchitsambamo nati, “Mose! Mose!” Ndipo anayankha, “Wawa.”


Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri.


Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira.


26 Yehova anayitana Mose mu tenti ya msonkhano. Iye anati,


Iyeyu anali mʼgulu la Aisraeli mʼchipululu pamodzi ndi mngelo amene anamuyankhula pa phiri la Sinai ndiponso makolo athu; ndipo Mose analandira mawu amoyo kuti atipatse ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa