Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwake magome awiri amiyala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwake magome awiri amiyala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Motero Mose adasema ina miyala iŵiri ngati yakale ija, ndipo kutacha m'maŵa, adakwera phiri la Sinai monga momwe Chauta adamlamulira. Anali atanyamula miyala iŵiri ija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:4
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.


Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti,


Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa.


Masiku aja Yehova anati kwa ine, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja, nukwere kuno kwa Ine m'phiri umu, nudzipangire likasa lamtengo.


Potero ndinapanga likasa la mtengo wakasiya, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa