Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Eksodo 18:23 - Buku Lopatulika Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mukachita zimenezi monga Mulungu akulamulira, simudzafooka, ndipo anthu onseŵa adzatha kumabwerera kwao, zao zonse zitakonzeka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.” |
Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa.
Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mzinda.
Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake.
Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.
Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri.
Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha.
ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.
Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.
Koma ndinakwera kunkako movumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwa amitundu; koma m'tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga chabe.
Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumzinda wake.