2 Samueli 18:3 - Buku Lopatulika3 Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mzinda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mudzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma anthuwo adati, “Inuyo simupita nao, chifukwa ife tikathaŵa, adani sadzatisamala. Ngati theka la ife lifa, iwo sadzasamalako za ife. Koma inu mukuposa anthu 10,000 mwa ife. Nchifukwa chake nkwabwino kwambiri kuti inu muzingotitumizira chithandizo kuchokera kumzindako.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Koma anthuwo anati, “Inu musapite nafe. Ngati tidzathamangitsidwa, iwowo sadzasamala za ife. Ngakhale theka la ife litafa, iwo sadzasamalako. Koma inuyo ndinu ofunika kuposa asilikali 10,000. Nʼkwabwino kwambiri kuti inu muzititumizira chithandizo kuchokera ku mzindako.” Onani mutuwo |