Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu inaima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu niima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mfumu idaŵauza kuti, “Chilichonse chimene chikukomereni, ndidzachita.” Choncho mfumuyo idakaimirira pambali pa chipata nthaŵi imene gulu lonse lankhondo linkatuluka mazanamazana, ndiponso zikwizikwi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mfumu inayankha kuti, “Ine ndichita chimene chili chokukomerani.” Kotero mfumu inayima pambali pa chipata pamene ankhondo onse amayenda mʼmagulu a anthu 100 ndi a 1,000.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:4
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.


Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.


Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.


ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata.


Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa