Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndipo mfumu idalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumlezere mtima mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.” Anthu onse adamva pamene mfumu inkalamula atsogoleri a ankhondo kunena za Abisalomu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mfumu inalamulira Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumukomere mtima Abisalomu chifukwa cha ine.” Ndipo asilikali onse anamva pamene mfumu imalamula izi za Abisalomu kwa wolamulira aliyense.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:5
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza.


Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.


Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.


Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu.


Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.


Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa