Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 18:2 - Buku Lopatulika

2 Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipo Davide adatumiza gulu lankhondo ataligaŵa patatu, chigawo chimodzi cholamulidwa ndi Yowabu, china cholamulidwa ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mng'ono wake wa Yowabu, china cholamulidwa ndi Itai Mgiti. Tsono mfumu idauza anthuwo kuti, “Inenso ndipita nao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Davide anatumiza asilikaliwo atawagawa patatu: gulu loyamba limalamulidwa ndi Yowabu, gulu lachiwiri limalamulidwa ndi Abisai ndipo gulu lachitatu limalamulidwa ndi Itai Mgiti. Mfumu inawuza asilikaliwo kuti, “Inenso ndipita nanu ndithu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 18:2
14 Mawu Ofanana  

Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.


Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele.


Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.


Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,


Ndipo mbiriyi inamfika Yowabu, pakuti Yowabu anapatukira kwa Adoniya, angakhale sanapatukire kwa Abisalomu. Ndipo Yowabu anathawira ku chihema cha Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe.


Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.


Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo.


Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao.


Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkutuluka m'mzinda; nawaukira iye nawakantha.


Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa