Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
Eksodo 16:23 - Buku Lopatulika Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziocha, ochani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ” |
Munatsikiranso paphiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera mu Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma;
ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.
musatulutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse.
Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,