Luka 23:56 - Buku Lopatulika56 Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201456 Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa56 Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero56 Kenaka anapita ku mudzi ndi kukakonza mafuta onunkhira. Koma anapuma pa tsiku la Sabata pomvera malamulo. Onani mutuwo |
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.