Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala mu Yerusalemu m'dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.
Eksodo 14:30 - Buku Lopatulika Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m'manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m'mphepete mwa nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m'manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m'mphepete mwa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku limenelo, Chauta adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito. Aisraele adaona Aejipitowo ali ngundangunda m'mbali mwa nyanja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku limeneli Yehova anapulumutsa Israeli mʼmanja mwa Aigupto ndipo Israeli anaona Aigupto ali lambalamba mʼmbali mwa nyanja atafa |
Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala mu Yerusalemu m'dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.
Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa.
Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.
Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ake, nati, Ali kuti Iye amene anawatulutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lake? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wake woyera pakati pao,
Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?
Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira.
Ndipo Yehova anati kwa ana a Israele, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti?
Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso mu Israele.
Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.