Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 91:8 - Buku Lopatulika

8 Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Uzingopenya ndi maso ako, ndipo udzaona m'mene amalangidwira anthu ochita zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Udzapenya ndi maso ako ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 91:8
9 Mawu Ofanana  

Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.


Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse.


Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m'manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m'mphepete mwa nyanja.


Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.


Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.


Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa