Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 10:19 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta adasintha mphepoyo kuti ikhale mphepo yamkuntho yakuzambwe, ndipo idapirikitsira dzombelo ku Nyanja Yofiira. Palibe dzombe ndi limodzi lomwe limene lidatsalako ku Ejipito kuja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo Yehova anasintha mphepo ija kuti ikhale ya mphamvu yochokera ku madzulo, ndipo inanyamula dzombe lija nʼkulikankhira mʼNyanja Yofiira. Panalibe dzombe ndi limodzi lomwe limene linatsala mu Igupto.

Onani mutuwo



Eksodo 10:19
7 Mawu Ofanana  

Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.


Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova.


Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele amuke.


Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.


Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.


koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu.


Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.