Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 10:19 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndipo Yehova anasintha mphepo ija kuti ikhale ya mphamvu yochokera ku madzulo, ndipo inanyamula dzombe lija nʼkulikankhira mʼNyanja Yofiira. Panalibe dzombe ndi limodzi lomwe limene linatsala mu Igupto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Chauta adasintha mphepoyo kuti ikhale mphepo yamkuntho yakuzambwe, ndipo idapirikitsira dzombelo ku Nyanja Yofiira. Palibe dzombe ndi limodzi lomwe limene lidatsalako ku Ejipito kuja.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:19
7 Mawu Ofanana  

Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe.


Mose anachoka kwa Farao nakapemphera kwa Yehova.


Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli apite.


Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo.


Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo Iye wawaponya mʼnyanja. Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao amizidwa mʼNyanja Yofiira.


“Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.


Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa