Yoweli 2:20 - Buku Lopatulika20 koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Ndidzachotsa adani akumpoto kuti akhale kutali ndi inu, ndipo ndidzaŵapirikitsira ku dziko louma ndi lachipululu. Akutsogolo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuvuma, akumbuyo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuzambwe. Tsono mitembo yao idzatulutsa chivundi ndi fungo lonunkha. Zoonadi Chauta adachita zazikulu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu. Onani mutuwo |