Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Danieli 4:5 - Buku Lopatulika Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndili chigonere pa bedi langa, ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Zinthu ndi masomphenya zimene ndinaziona zinandiopsa. |
Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.
Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.
Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati padziko lapansi, msinkhu wake ndi waukulu.
Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.
Koma siyani chitsa ndi mizu yake m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo; nchokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zili m'machire a m'dziko.
Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.
Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike;
pali munthu mu ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;
Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.
Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga.