Danieli 4:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Ndili chigonere pa bedi langa, ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Zinthu ndi masomphenya zimene ndinaziona zinandiopsa. Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine. Onani mutuwo |
Pamenepo Danieli, amene amatchedwa Belitesezara, anavutika mu mtima kwambiri kwa kanthawi, ndipo anasautsidwa mʼmaganizo ake. Choncho mfumu inati, “Belitesezara usalole malotowa kapena tanthauzo lake likuopse.” Belitesezara anayankha kuti, “Mbuye wanga, ndikanakonda malotowa akanakhudza adani anu okha, ndi tanthauzo lake kwa iwo okusautsani!
Pali munthu wina mu ufumu wanu uno amene mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera. Pa nthawi ya ulamuliro wa abambo anu iye anapezeka kuti ali ndi chidziwitso, luntha ndi nzeru zonga za milungu. Mfumu Nebukadinezara, abambo anu, Ine ndikukuwuzani anamusankha iye kukhala mkulu wa amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula.