Danieli 4:13 - Buku Lopatulika13 Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 “Ndikanali chigonere ndinaona mʼmasomphenya mngelo atayima pamaso panga, woyera, atatsika kuchokera kumwamba. Onani mutuwo |
Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo, ndipo chikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zakuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;