Danieli 4:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 “Ndikanali chigonere ndinaona mʼmasomphenya mngelo atayima pamaso panga, woyera, atatsika kuchokera kumwamba. Onani mutuwoBuku Lopatulika13 Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. Onani mutuwo |
“Inu mfumu munaona mthenga woyera, akuchokera kumwamba ndipo anati, ‘Gwetsani mtengo ndipo muwuwononge, koma musiye tsinde ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi unyolo wa chitsulo ndi mkuwa ndipo mulisiye pakati pa udzu wa mʼmunda. Mulole kuti linyowe ndi mame akumwamba. Likhale ngati nyama zakuthengo, mpaka zaka zidutse zisanu ndi ziwiri.’
Kenaka ndinamva wina akuyankhula; ndipo woyera winanso anamufunsa kuti, “Kodi zimene ndikuziona mʼmasomphenyazi zidzatha liti? Nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku zidzakhala zoletsedwa mpaka liti? Nanga chonyansa chosokoneza chidzakhalapo mpaka liti? Kodi gulu la ankhondo lidzapondereza malo opatulika mpaka liti?”