Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.
Danieli 2:11 - Buku Lopatulika Pakuti chinthu achifuna mfumu nchapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuchiwulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti chinthu achifuna mfumu nchapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuchiwulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.” |
Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.
Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.
Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?
Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.
Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.
Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m'nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m'chinyumba changa.
pali munthu mu ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli;
Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele.
Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.
Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.
ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.
Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;