Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 2:12 - Buku Lopatulika

12 Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse mu Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse m'Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 2:12
14 Mawu Ofanana  

Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.


Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; wanzeru adzaukhulula.


Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu.


Kuopsa kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango; womputa achimwira moyo wakewake.


Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa.


Potero Daniele analowa kwa Ariyoki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babiloni; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babiloni, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.


Niyankha mfumu, niti kwa Ababiloni, Chandichokera chinthuchi; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.


Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi mu ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.


Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anasandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.


ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.


Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa