Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 12:6 - Buku Lopatulika

Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mmodzi mwa awiriwo anafunsa munthu wovala chovala chosalala amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja kuti, “Kodi padzapita nthawi yayitali bwanji kuti zodabwitsazi zidzakwaniritsidwe?”

Onani mutuwo



Danieli 12:6
16 Mawu Ofanana  

Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.


Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya chipata cha kumtunda choloza kumpoto, aliyense ndi chida chake chophera m'dzanja lake; ndi munthu mmodzi pakati pao wovala bafuta, ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.


Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija.


Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?


Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?


Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabriele, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.


Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?


Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?


kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


ndipo anatuluka mu Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao.


Ndipo magulu a nkhondo okhala mu Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu.


ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?