Danieli 12:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Mmodzi mwa awiriwo anafunsa munthu wovala chovala chosalala amene anali mʼmbali mwa madzi a mu mtsinje uja kuti, “Kodi padzapita nthawi yayitali bwanji kuti zodabwitsazi zidzakwaniritsidwe?” Onani mutuwoBuku Lopatulika6 Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti? Onani mutuwo |
Kenaka ndinamva wina akuyankhula; ndipo woyera winanso anamufunsa kuti, “Kodi zimene ndikuziona mʼmasomphenyazi zidzatha liti? Nsembe zoperekera machimo za tsiku ndi tsiku zidzakhala zoletsedwa mpaka liti? Nanga chonyansa chosokoneza chidzakhalapo mpaka liti? Kodi gulu la ankhondo lidzapondereza malo opatulika mpaka liti?”
Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.