Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamene Yesu anakhala pansi pa phiri la Olivi, ophunzira ake anabwera kwa Iye mwamseri nati, “Tiwuzeni, kodi izi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kubwera kwanu ndi zizindikiro za kutha kwa dziko zidzakhala chiyani?”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:3
23 Mawu Ofanana  

Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.


Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino,


Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho?


Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.


Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoze bwanji kuchitulutsa?


Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,


Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike?


Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa Iye yekha.


chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa