Danieli 12:13 - Buku Lopatulika Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Koma iweyo Danieli, pitiriza ndipo ulimbikire mpaka matsiriziro. Kenaka udzamwalira. Koma mʼmasiku otsiriza udzauka kuti ulandire gawo lako.” |
Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.
Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.
Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.
Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo.
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.
Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.
Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.
ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.