Zekariya 3:7 - Buku Lopatulika7 Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 “Zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, ‘Mukamayenda m'njira yanga, ndi kumamveradi malamulo anga, mudzalamulira m'nyumba mwanga, ndipo mudzayang'anira mabwalo anga. Tsono ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi aŵa ali panoŵa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa. Onani mutuwo |