Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 3:8 - Buku Lopatulika

8 Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsopano imva, iwe Yoswa, mkulu wa ansembe, imvani nanunso ansembe anzakenu, amene muli chizindikiro cha zabwino zimene zidzachitike. Ndidzabwera naye mtumiki wanga wotchedwa dzina loti “Nthambi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “ ‘Mvera tsono, iwe Yoswa mkulu wa ansembe, pamodzi ndi anzako amene wakhala nawowa, amene ndi chizindikiro cha zinthu zimene zikubwera: Ine ndidzabweretsa mtumiki wanga, wotchedwa Nthambi.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 3:8
24 Mawu Ofanana  

Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba.


Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso;


Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya;


Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, amene ndidzalemekezedwa nawe.


Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wake, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israele asonkhanidwe kwa Iye; chifukwa Ine ndili wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;


Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.


Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.


Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.


Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.


Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.


Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dzikomu.


Uziti, Ine ndine chizindikiro chanu, monga ndachita ine momwemo kudzachitidwa nao; adzachotsedwa kunka kundende.


Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwatulutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika chizindikiro cha nyumba ya Israele.


Momwemo Ezekiele adzakhala kwa inu chizindikiro; umo monse anachitira iye mudzachita ndinu; chikadza ichi mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.


Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.


Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita.


nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova:


chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa