Mateyu 19:28 - Buku Lopatulika28 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201428 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa28 Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu akadzakonzanso zinthu zonse, Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake wachifumu ndi waulemerero. Tsono inunso amene mudanditsatanu, mudzakhala pa mipando yachifumu khumi ndi iŵiri mukuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero28 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.