Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
Danieli 10:14 - Buku Lopatulika Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.” |
Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.
Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali.
ndipo udzakwerera anthu anga Israele ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzachitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.
Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.
Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.
koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa:
Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabriele, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo.
Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.
Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Daniele iwe, ndatuluka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha.
atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.
Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.
Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.
Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzachitira anthu anu, masiku otsiriza.
Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira.
Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu.
Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ake;
tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;