Mika 4:1 - Buku Lopatulika1 Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pa masiku akudzaŵa, phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse. Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko. Onani mutuwo |
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.