Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Ahebri 2:8 - Buku Lopatulika

mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyepo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayambe tsopano apa kuona zonse zimgonjera.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyapo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayamba tsopano apa kuona zonse zimgonjera.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

ndipo mudampatsa ulamuliro pa zinthu zonse.” Tsono ngati Mulungu adapatsa munthu ulamuliro pa zinthu zonse, palibe kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Komabe m'mene zinthu ziliri tsopano sitikuwona kuti zonse zakhaladi mu ulamuliro wakewo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Munamupatsa ulamuliro pa zinthu zonse.” Poyika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, Mulungu sanasiye kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Koma nthawi ino sitikuona zinthu pansi pa ulamuliro wake.

Onani mutuwo



Ahebri 2:8
19 Mawu Ofanana  

Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,


Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake.


Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.


Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?


koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;


Pakuti sanagonjetsere angelo dziko lilinkudza limene tinenali.


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;