Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 1:13 - Buku Lopatulika

13 Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala pa dzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti, “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditapanga adani ako kukhale chopondapo mapazi ako.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 1:13
16 Mawu Ofanana  

Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja lamanja langa, kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.


Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalimo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja langa lamanja,


Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana aamuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa