Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Ahebri 10:4 - Buku Lopatulika

Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Magazi a ng'ombe zamphongo ndi a atonde sangathe konse kuchotsa machimo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

Onani mutuwo



Ahebri 10:4
19 Mawu Ofanana  

Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.


Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.


Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.


ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.


M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo, pamene ndidzachotsa machimo ao.


Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.


Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;


Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifune, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),


ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.


Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.