Ahebri 10:8 - Buku Lopatulika8 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifune, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo), Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo), Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Motero poyamba adati, “Nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zoperekera machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo.” Zimenezi nzimene Malamulo adaanena kuti ziperekedwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. Onani mutuwo |