Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.
Afilipi 1:13 - Buku Lopatulika kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m'bwalo lonse la alonda, ndi kwa ena onse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m'bwalo lonse la alonda, ndi kwa onse ena; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwakuti asilikali onse olonda nyumba ya mfumu, ndi ena onse kuno, adziŵa kuti ndili m'ndende chifukwa cha Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chotsatira chake nʼchakuti zadziwika bwino lomwe kwa onse amene ali ku nyumba yaufumu kuti ine ndili mʼmaunyolo chifukwa cha Khristu. |
Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi.
ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzake, nanena, Munthu uyu sanachite kanthu koyenera imfa, kapena nsinga.
Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma;
Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu.
Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye,
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.
ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine.
monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.
m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika.