Aefeso 4:2 - Buku Lopatulika ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. |
Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.
Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.
wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda;
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.
chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.
olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,
Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.
wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,
Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.
koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;