Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine.
3 Yohane 1:7 - Buku Lopatulika pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja adaanyamuka ulendo wao chifukwa cha dzina la Khristu, osalandira thandizo kwa akunja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ananyamuka ulendo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye, osalandira thandizo kwa osakhulupirira. |
Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine.
M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.
Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.
pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.
Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.
Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi.
Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.
Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;
Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.