Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




3 Yohane 1:6 - Buku Lopatulika

6 amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Iwo adachitira umboni chikondi chako pamaso pa mpingo. Ndi bwinodi kuti uŵathandize mokondweretsa Mulungu kupitiriza ulendo wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo anafotokozera mpingo za chikondi chako. Chonde uwathandize kupitiriza ulendo mʼnjira yokondweretsa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




3 Yohane 1:6
15 Mawu Ofanana  

Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.


Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?


kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.


Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.


Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mzinda; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera,


pamene paliponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.


ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.


Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa.


kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;


ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.


Zena nkhoswe ya milandu, ndi Apolo ufulumire kuwakonzera zaulendo, kuti asasowe kanthu,


Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.


Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa