Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




3 Yohane 1:7 - Buku Lopatulika

7 pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Paja adaanyamuka ulendo wao chifukwa cha dzina la Khristu, osalandira thandizo kwa akunja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pakuti ananyamuka ulendo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye, osalandira thandizo kwa osakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




3 Yohane 1:7
17 Mawu Ofanana  

Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine.


Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.


M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.


Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.


Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.


pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa.


Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.


Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi.


Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu.


Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,


Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;


Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.


ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa