3 Yohane 1:11 - Buku Lopatulika Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuone Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuona Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wokondedwa, usamatsanzire zoipa, koma zabwino. Aliyense wochita zabwino, ndi mwana wa Mulungu, koma wochita zoipa, sadaone Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wokondedwa, usatsatire zinthu zoyipa koma zinthu zabwino. Aliyense amene amachita zinthu zabwino ndi wochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amachita zoyipa sanamuonepo Mulungu. |
Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu;
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.
Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.
Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.
Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera;
Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala mu Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda;
Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro,
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.
Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino?
Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.
M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.