Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
2 Samueli 5:6 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sangathe kulowa muno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mfumu Davide ndi anthu ake adapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi. Ayebusiwo anali nzika za dzikolo. Anthuwo adauza Davide kuti, “Sudzaloŵa muno ai. Anthu akhungu ndi anthu opunduka ndiwo adzakupirikitse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.” |
Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu.
Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?
Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mzinda uwu ndi moto.
Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,
Chifukwa chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piramu mfumu ya Yaramuti, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Debiri mfumu ya Egiloni, ndi kuti,
Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.
Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala mu Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala mu Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.
Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mzinda ndi moto.