Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 5:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sangathe kulowa muno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mfumu Davide ndi anthu ake adapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi. Ayebusiwo anali nzika za dzikolo. Anthuwo adauza Davide kuti, “Sudzaloŵa muno ai. Anthu akhungu ndi anthu opunduka ndiwo adzakupirikitse.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 5:6
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba,


Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.


Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.


Ndidzalimbana nanu, inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa, inu okhala ngati thanthwe lapachidikha, akutero Yehova. Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe? Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’


Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”


Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa.


Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni.


Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.


Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake. Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.


Koma fuko la Benjamini linalephera kuwachotsa Ayebusi, amene amakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusiwo akukhalabe ndi fuko la Benjamini mu Yerusalemu mpaka lero.


Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa