Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 1:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mzinda ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pambuyo pake Ayuda adathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, naulanda. Adapha anthu ambiri, natentha mzinda wonsewo ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 1:8
3 Mawu Ofanana  

Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.


Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala mu Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala mu Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.


Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa