Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira.
2 Samueli 22:39 - Buku Lopatulika Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka, inde anagwa pansi pa mapazi anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka, inde anagwa pansi pa mapazi anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidaŵakantha, ndidaŵagwetsa pansi, kotero kuti sadadzukenso, ndidaŵapondereza ndi mapazi anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga. |
Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira.
Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema.
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.
Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana aamuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.