Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.
2 Samueli 22:18 - Buku Lopatulika Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane; pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga amene anali amphamvu kuposa ine. |
Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.
amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;
Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.