Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 21:9 - Buku Lopatulika

niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

naŵapereka kwa Agibiyoni. Tsono onsewo adaŵanyonga pa phiri, pamaso pa Chauta, ndipo asanu ndi aŵiri onsewo adafera pamodzi. Iwowo adaphedwa masiku oyamba akholola, nthaŵi yoyamba kudula barele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele.

Onani mutuwo



2 Samueli 21:9
13 Mawu Ofanana  

Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.


Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.


Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa.


Koma tirigu ndi rai sizinayoyoke popeza amabzala m'mbuyo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele.


Munthu akakhala nalo tchimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampachika;


Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.


Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.