Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 21:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

9 niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 naŵapereka kwa Agibiyoni. Tsono onsewo adaŵanyonga pa phiri, pamaso pa Chauta, ndipo asanu ndi aŵiri onsewo adafera pamodzi. Iwowo adaphedwa masiku oyamba akholola, nthaŵi yoyamba kudula barele.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 21:9
13 Mawu Ofanana  

mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.” Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”


Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.


Davide anamuyankha Mikala kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Yehova, amene anandisankha ine kupambana abambo ako, kapenanso kupambana banja la abambo ako. Ndipo anandisankha kuti ndikhale wolamulira Aisraeli, anthu a Yehova. Nʼchifukwa chake ndidzasangalalabe pamaso pa Yehova.


Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.


Thonje ndi barele zinawonongeka, popeza barele anali atakhwima ndi thonje linali ndi maluwa.


Koma tirigu ndi mchewere sizinawonongeke chifukwa zimakhwima mochedwa.


Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga atsogoleri onse a anthu awa, uwaphe poyera, pamaso pa Yehova kuti mkwiyo waukulu wa Yehova uchoke pa Israeli.”


Ngati munthu wopezeka ndi mlandu wopha mnzake waphedwa ndipo mtembo wake wapachikidwa pamtengo,


Naomi anabwerera kuchoka ku dziko la Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake. Ndipo anafika ku Betelehemu nthawi yoyamba kukolola barele.


Koma Samueli anati, “Monga momwe lupanga lako linasandutsira amayi kukhala wopanda ana, momwemonso amayi ako adzakhala opanda mwana pakati pa amayi.” Ndipo Samueli anapha Agagi pamaso pa Yehova ku Giligala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa