2 Samueli 21:6 - Buku Lopatulika6 Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Mutipatse ana ake amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova m'Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono mwa zidzukulu zake mutipatse anthu asanu ndi aŵiri, kuti ife tikaŵanyonge pamaso pa Chauta ku Gibiyoni, ku mzinda wa Saulo munthu wosankhidwa wa Chauta.” Apo mfumuyo idayankha kuti, “Chabwino, ndidzaŵapereka.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.” Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.” Onani mutuwo |