2 Samueli 21:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalole mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo zakuthengo usiku. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo za kuthengo usiku. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Tsono Rizipa, mwana wamkazi wa Aya, adatenga chiguduli nadziyalira pathanthwe pamene panali mitembo ya anthuwo, kuyambira pa chiyambi cha kholola mpaka mvula idayambanso kugwa. Mkaziyo sadalole kuti pa mitemboyo pafike mbalame masana kapena zilombo zakuthengo usiku. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku. Onani mutuwo |