Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
2 Samueli 21:22 - Buku Lopatulika Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu anaiwo anali zidzukulu za Arefaimu a ku Gati, ndipo adaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu anayi amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo onse anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake. |
Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
Awa anabadwa mwa chimphonacho ku Gati, koma anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.
M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:
Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake.
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;
Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi mizinda yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova.