Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 20:23 - Buku Lopatulika

Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yowabu ankalamulira gulu lonse lankhondo la Aisraele. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, ankalamulira Akereti ndi Apeleti.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yowabu ndiye amalamulira gulu lonse la ankhondo. Benaya mwana wa Yehoyada amalamulira Akereti ndi Apeleti.

Onani mutuwo



2 Samueli 20:23
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka namtsata anthu a Yowabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onse amphamvu; natuluka mu Yerusalemu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.


Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;


Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse.


Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.


Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.


Ndipo mfumu Solomoni anali mfumu ya Israele yense.


Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.